Chinenero chamakono: ny Chichewa

Zinenero
Selected Language:

Aphunzitsi Athu

Modzazidwa ndi kulimba mtima ndi chikhumbokhumbo, John Bevere ndiye mlembi wa mabuku ogulitsidwa kwambiri monga Za Chilendo (Extraordinary), Nyambo ya Mdierekezi (The Bait of Satan), Kuopa Mulungu (The Fear of the Lord), Chobisika (Under Cover), ndi Kuyendetsedwa ndi Muyaya (Driven by Eternity). Mabuku ake atanthauzidwa m’zinenero zoposa zana, ndipo weekly television program yake, The Messenger, imaulutsidwa kuzungulira dziko lapansi. John ndiye wolankhula wotchuka pa misonkhano ndi m’mipingo, ndipo utumiki wake umapereka zipangizo zosintha umoyo kwa iwo amene akufuna kumvetsa ndi kugwiritsa ntchito fundo za Mulungu. John amakonda kukhala ku Colorado Springs ndi mkazi wake, Lisa, amenenso ali wolemba mabuku ogulitsidwa kwambiri komanso wolankhula wotchuka,ndi ana awo anayi, mpongozi wawo, ndi adzukulu awo.

Onani Zipangizo Zotengedwa Zomwe Zilipo Email John Bevere

Wa chikhumbokhumbo. Wodera Nkhawa. Wokambika. Wamphamvu. Wosangalatsa. Mawu awa amafotokozera za Lisa Bevere-wolankhula ku dziko lonse, wolemba mabuku ogulitsidwa kwambiri, ndi wochita nawo The Messenger International program, yomwe imaulutsidwa m’maiko oposa mazana awiri. M’machitidwe ake oonekera, Lisa akugawana Mawu a Mulungu olumikizidwa ndi zochitika zomwe amakumana nazo zopereka mphamvu, ufulu ndi kusintha ku moyo. Monga woimira chilungamo, amalimbikitsa ena kuti akhale yankho la mavuto aakulu a pafupi ndi a kutali. Amakonda kukhala ndi nthawi ya kucheza ndi wokondedwa wake, mwamuna wake John Bevere, ndi ana awo anayi, mpongozi wake wodabwitsa, ndi adzukulu awo osiririka.

Onani Zipangizo Zotengedwa Zomwe Zilipo Email Lisa Bevere