Chinenero chamakono: ny Chichewa

Zinenero

Mudzi - Mabuku - Kupha Chofooketsa

Kupha Chofooketsa
Mphunzitsi: John Bevere
Akupezeka m’chinenero:

Ukhoza Kuwononga Chomwe Chimaba Mphamvu Yako

Monga Superman, amene akhoza kudumpha vuto liri lonse ndi kugonjetsa mdani ali yense, wotsatira Kristu ali ndi mphamvu yapadera yogonjetsa zovuta zomwe timakumana nazo. Koma vuto la Superman ndi ife ndilakuti, pali chofooketsa (kryptonite) chomwe chimaba mphamvu zathu.

Zowonadi, Superman ndi kryptonite ndi zongopeka. Koma kryptonite ya uzimu siyili motero.

Buku ili limapereka mayankho a chifukwa chake ambiri a ife sitingathe kuwona mphamvu ya umulungu imene inkawonekera pakati pa Akristu oyambirira.

Mu Kupha Chofooketsa, John Bevere akuwulula momwe chofooketsa (kryptonite) ichi chiliri, momwe chimasokonezera m’magulu athu, ndi momwe tingamasukire ku ukapolo wa icho.

Osati kwa ozilara mtima, Kupha Chofooketsa sichina ayi, koma uzimu wonyanyitsa. Ichi ndi chowonadi chenicheni kwa ali yense wotsata Kristu amene akulakalaka kulandira njira yovuta koma yopindulitsa ya kusintha.

Zipangizo Zina za Ndondomeko ya Phunziroli:
Kupha Chofooketsa Buku la Uthenga Womvestera

Tengani (~2.27 MB)

Gawirani pa