Mudzi - Mabuku - Chabwino Kapena Mulungu?

Chabwino Kapena Mulungu?
Mphunzitsi: John Bevere

Chifukwa chimene Chabwino chopanda Mulungu chili chosakwanira

Ngati nchabwino, chiyenera kukhala Mulungu. Ndi momwemo kodi?

Masiku ano, mawu awa Chabwino.ndi Mulunguamakhala ngati ofanana. Tikhulupirira kuti nthawi zambiri chimene chili chovomerezeka kuti ndi chabwino, chiyenera kukhala m’chifuniro cha Mulungu. Kukoma mtima, kudzichepetsa, chilungamo—chabwino, kudzikonda, kudzikweza, kuipa mtima—choipa. Kusiyana kwake kuoneka ngati ndi kwa pafupi.

Koma ndi zokhazo pa ichi kodi? Ngati chabwino chili cha chidziwikire, nanga bwanji Buku Lopatulika linena kuti pafunika kufatsa bwino kuti timvetsetse za ichi?

Chabwino Kapena Mulungu? si uthenga wongodzithandiza. Bukuli lidzachita zazikulu zoposa osati kungokusinthani chabe khalidwe lanu. Lidzakupatsani mphamvu ya kuchita ndi Mulungu koposa ndiponso mudzasintha mbali zonse za umoyo wanu.

Tengani (~2.88 MB)

Gawirani pa