Mudzi - Mabuku - Mulungu Muli Kuti?!

Mulungu Muli Kuti?!
Mphunzitsi: John Bevere

Kupeza Mphamvu ndi Cholinga M’chipululu Chanu

Kodi mumamva ngati mwataika m’nyengo m’nyengo yamavuto, mukusinkhasinkha, “MULUNGU, MULI KUTI?!”

Mwina mwake munamva Mulungu akulankhula, koma tsopano akuoneka ngati waleka. Mwina munapita patsogolo m’chikhulupiriro, koma tsopano nkhope Yake sikupezeka. Mwalandiridwa ku chipululu—malo amene ali pakati polandira lonjezo lochokera kwa Mulungu ndikuona likukwaniritsidwa.

Koma nkhani yabwino ndi iyi—awa simalo opanda cholinga. Mulungu amagwiritsa ntchito chipululu kukukonzani ndi kupereka zofunikira zatsogolo lanu—ngati mungazigwiritse ntchito molondola. Mosiyana ndi m’mene ambiri angaganizire, kudutsa m’nyengo iyi sikungodikira Mulungu kokha. Muli ndi gawo logwiritsira ntchito podutsa m’menemo. Gawo lalikulu. Ndipo ngati simufuna kutaya nthawi pomangozungulira, nkofunika kuphunzira za chimenechi.

M’buku lozindikiritsali, katswiri wolemba mabuku John Bevere akukupatsani zofunikira ndi fundo za zikuluzikulu za m’Baibulo komanso nkhani zozama zimene zidzakuthandizani kuyenda m’nyengo zanu zouma komanso zovuta ndi kulowa mu zonse zimenee Mulungu anakusungirani.

Tengani (~1.55 MB)

Gawirani pa