Chinenero chamakono: ny Chichewa

Zinenero
Selected Language:

Mudzi - Mabuku - Kutsogoleredwa ndi Muyaya

Kutsogoleredwa ndi Muyaya
Mphunzitsi: John Bevere
Akupezeka m’chinenero:

Moyo uwu wa padziko lapansi uli ngati utsi, komabe ambiri a ife timakhala ngati kuti palibenso china kumbali ina. Koma momwe timakhalira moyo uno kudzapangitsa m’mene tidzakhalira kwa muyaya. Lembo limatiuza kuti padzakhala magawo osiyanasiyana a mphotho kwa okhulupilira-kuyambira kuonera zonse zomwe munthu analimbikira zikusakazidwa mu chiweruzo, mpaka kukalamulira pamodzi ndi Kristu Mwini wake.

Pogwiritsa ntchito fundo za pa 2 Akorinto 5:9-11, John Bevere akutikumbutsa kuti okhulupirira onse adzaima pa maso pa Kristu kuti alandire zomwe adapeza m’moyo. Ambiri a ife tidzadabwa podziwa kuti nthawi yathu yambiri inathera pa zinthu zopanda ntchito pa zokhudza mphotho zosatha.

Ndiye tingatani kuti tikhale ndi moyo wa tanthauzo? Mu Kuyendetsedwa ndi Muyaya, mudzaphunzira kupeza mayitanidwe anu ndi kuchulukitsa zomwe Mulungu anakupatsani. Pamene mukupeza malingliro osatha, mudzakhala ndi mphamvu yogwira ntchito ku zinthu zokhalitsa.

Tengani (~3.47 MB)

Gawirani pa