Chinenero chamakono: ny Chichewa

Zinenero
Selected Language:

Mudzi - Za

Za Cloud Library

Messenger International ali ndi cholinga chodzipereka padziko lapansi kuti apange zinthu izi kwa abusa ndi atsogoleri mosadera nkhawa malo kapena ndalama. Cloud Library inapangidwa chifukwa cha ichi. Imatumikira ngati mlato wofalitsa wa padziko lonse womwe umalola kuti zinthu zotanthauzidwa zipezeke mosefukira ndi kutengedwa kwaulere.

Cholinga chathu ndikupanga zipangizozi kuti zikhalepo m’zinenero zonse zazikuluzikulu, motero ndi kukhazikitsa mwayi wofikira anthu oposa 98% adziko lapansi. Cloud Library ndi njira imodzi yokwaniritsira cholinga ichi. Bwanji, mukhoza kufunsa? Chifukwa chipangizo chophweka chingathe kuchulukana ndi kuyenda mofulumira kwambiri kusiyana ndi chogwirika. Tikukhulupirira kuti musangalala ndi zomwe mukumane nazo mu cloud.

Kuchokera kwa Olenga

Yesu anatilamulira ife osati kungolalikira kokha uthenga wabwino, komanso kuti titukule ophunzira. Ma uthenga awa adzakuthandizani kukhala ophunzira a Kristu. Tikukuphunzitsani chifukwa timakhulupirira mwa inu ndi luso lanu, mwa chisomo cha Mulungu, kuti musinthe ku malo kumene muli ndi ulamuliro. Mulungu waika ukulu mkati mwanu, ndipo amalakalaka kukudziwani bwino. Zipangizo izi zidzakuthandizani kupeza ubale wa pamtima ndi Mulungu. Pamene mukukula mu ubale wanu ndi Kristu, mudzasinthidwa ndi mphamvu ya Mau Ake.

Mulungu anakulengani ndi cholinga chosiyana ndi cha wina ali yense koma choyenderana ndi mphatso ndi chikoka chanu. Tikukulimbikitsani kuti mufufuze mozama chiri chonse chomwe Mulungu ali nacho kwa inu. Pemphero lathu ndi loti zipangizo izi zidzakhala zida zanu pa ulendo wanu wokaunikiridwa.

Madalitso kwa inu ndi yanu,

John & Lisa Bevere

Thandizani Masomphenya

Kodi mtima wanu umatentha kuona zipangizo zosintha moyo zomwe zagawidwa padziko lonse lapansi? Ngati muli wokondweretsedwa pothandiza ntchito ya Cloud Library, chonde tumizani mawu ku getinvolved@cloudlibrary.org. Tikukuthokozeranitu chifukwa cha mapemphero ndi mathandizo anu!